Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • Ekisodo 4:21
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 21 Yehova anauzanso Mose kuti: “Ukakafika ku Iguputo ukaonetsetse kuti wachita pamaso pa Farao,+ zozizwitsa zonse zimene ndakulola kukachita. Ndipo ine ndidzamusiya kuti aumitse mtima wake,+ moti sadzalola anthu anga kuchoka.+

  • 1 Samueli 6:6
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 6 Komanso, mukuumitsiranji mitima yanu mmene Aiguputo ndi Farao anaumitsira mitima yawo?+ Si paja Mulungu atangowakhaulitsa+ analola Aisiraeli kupita, ndipo iwo anapitadi?+

  • Yobu 9:4
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    •  4 Iye ali ndi mtima wanzeru ndiponso mphamvu zambiri.+

      Ndani angachite naye makani,* koma osavulala?+

  • Miyambo 29:1
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 29 Munthu wodzudzulidwa kawirikawiri+ koma amene amaumitsa khosi lake,+ adzathyoledwa mwadzidzidzi ndipo akadzatero sadzachira.+

  • Danieli 5:20
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 20 Koma pamene mtima wake unayamba kudzitukumula ndiponso pamene anaumitsa mtima wake ndi kuchita zinthu modzikweza,+ anatsitsidwa pampando wake wachifumu ndipo ulemerero wake unachotsedwa.+

  • Aroma 9:18
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 18 Chotero, iye amachitira chifundo munthu amene wafuna kumuchitira chifundo,+ koma amalola anthu ena kuti aumitse mitima yawo.+

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena