8 “‘Usadzipangire fano+ kapena chifaniziro+ cha chinthu chilichonse chakumwamba, kapena chapadziko lapansi, kapenanso cha m’madzi a pansi pa dziko lapansi.*
29 “Popeza kuti ndife mbadwa za Mulungu,+ tisaganize kuti Mulunguyo+ ali ngati golide, siliva, mwala kapena chilichonse chosemedwa mwa luso ndi nzeru za munthu.+
4 Ndiyeno pa nkhani ya kudya+ zakudya zoperekedwa kwa mafano, timadziwa kuti fano ndi lopanda pake+ m’dziko, ndiponso kuti kulibe Mulungu wina koma mmodzi yekha.+
20 Koma anthu ena onse amene sanaphedwe ndi miliri imeneyi, sanalape ntchito za manja awo.+ Sanalape kulambira ziwanda+ ndi mafano agolide, asiliva,+ amkuwa, amwala, ndi amtengo, mafano amene sangathe kuona, kumva, kapena kuyenda.+