Levitiko
2 “‘Munthu akafuna kupereka nsembe yambewu+ kwa Yehova, nsembe yakeyo izikhala ufa wosalala.+ Azithira mafuta ndi kuika lubani* pa ufawo. 2 Akatero azibweretsa nsembe yakeyo kwa ana a Aroni, ansembe. Ndipo wansembe azitapa ufa wothira mafutawo pamodzi ndi lubani yense kudzaza dzanja limodzi, ndi kuutentha paguwa lansembe kuti ukhale chikumbutso+ cha nsembeyo. Imeneyi ndi nsembe yotentha ndi moto, yafungo lokhazika mtima pansi kwa Yehova. 3 Ndipo zotsala za nsembe yambewu ndi za Aroni ndi ana ake,+ popeza ndi zopatulika koposa,+ zochokera pansembe zotentha ndi moto zoperekedwa kwa Yehova.
4 “‘Ngati mukupereka nsembe yambewu yophikidwa mu uvuni, izikhala ya ufa wabwino kwambiri. Muzipereka mkate wozungulira woboola pakati,+ wopanda chofufumitsa, wothira mafuta, kapena timitanda ta mkate topyapyala topanda chofufumitsa,+ topaka mafuta.+
5 “‘Ngati mukupereka nsembe yambewu yophika m’chiwaya,+ izikhala ya ufa wabwino kwambiri wothira mafuta, yopanda chofufumitsa. 6 Muziibenthula zidutswazidutswa ndi kuithira mafuta.+ Imeneyi ndi nsembe yambewu.
7 “‘Ngati mukupereka nsembe yambewu yophika mumphika wa mafuta ambiri, izikhala yopangidwa ndi ufa wosalala ndiponso mafuta. 8 Ndipo nsembe yambewu yopangidwa moteremu muzibwera nayo kwa Yehova. Muziipereka kwa wansembe, ndipo iye azipita nayo paguwa lansembe. 9 Kenako wansembe azitengako pang’ono nsembe yambewu kuti ikhale chikumbutso,+ ndipo azitentha zimene watengazo paguwa lansembe. Imeneyi ndi nsembe yotentha ndi moto, yafungo lokhazika mtima pansi kwa Yehova.+ 10 Ndipo zotsala za nsembe yambewu ndi za Aroni ndi ana ake, popeza ndi zopatulika koposa zochokera pansembe zotentha ndi moto zoperekedwa kwa Yehova.+
11 “‘Nsembe yambewu imene mudzapereka kwa Yehova ikhale yopanda chofufumitsa,+ chifukwa simuyenera kutentha mtanda wofufumitsa wa ufa wokanda ndiponso uchi,* monga nsembe yotentha ndi moto yoperekedwa kwa Yehova.
12 “‘Zimenezi mudzazipereka kwa Yehova monga nsembe ya zipatso zoyambirira,+ chotero simuyenera kuzibweretsa paguwa lansembe kuti zikhale nsembe yafungo lokhazika mtima pansi.
13 “‘Nsembe yanu iliyonse yambewu muziikoleretsa ndi mchere.+ Musapereke nsembe yanu yambewu yopanda mchere wokukumbutsani pangano+ la Mulungu. Popereka nsembe yanu iliyonse muziperekanso mchere.
14 “‘Ngati mukupereka kwa Yehova nsembe yambewu ya zipatso zoyambirira kucha,+ muzipereka tirigu* wamuwisi wotibula, wokazinga pamoto, kuti akhale nsembe yambewu ya zipatso zanu zoyambirira kucha. 15 Muzithira mafuta ndi kuika lubani pansembeyo. Imeneyi ndi nsembe yambewu.+ 16 Ndipo wansembe azitentha chikumbutso+ cha nsembeyo, kapena kuti, tirigu wotibula uja pang’ono ndi mafuta, pamodzi ndi lubani wake yense, kuti zikhale nsembe yotentha ndi moto yoperekedwa kwa Yehova.