16 Amenewa ndi operekedwa. Aperekedwa kwa ine kuchokera pakati pa ana a Isiraeli.+ Ine ndikuwatenga iwowa m’malo mwa onse otsegula mimba ya mayi awo, oyamba kubadwa onse pakati pa ana a Isiraeli.+
6 Inetu ndatenga abale anu Alevi, mwa ana a Isiraeli,+ ndipo ndawapereka kwa inu monga mphatso yanu.+ Iwowa akhala operekedwa kwa Yehova kuti atumikire pachihema chokumanako.+