23 Yosefe anakhalabe ndi moyo mpaka kuona ana a Efuraimu a m’badwo wachitatu.+ Anaonanso ana a Makiri+ mwana wa Manase. Onsewo anabadwira pamiyendo pa Yosefe.+
36Atsogoleri a mabanja a ana a Giliyadi mwana wa Makiri,+ mwana wa Manase, ochokera kumabanja a ana a Yosefe, anafika ndi kulankhula ndi Mose ndi akalonga omwe anali atsogoleri a ana a Isiraeli.