Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • Genesis 29:35
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 35 Anakhalanso ndi pakati pena n’kubereka mwana wamwamuna, ndipo anati: “Tsopano nditamanda Yehova.” Choncho Leya anatcha mwanayo, Yuda.*+ Atabereka mwana ameneyu, anayamba waleka kubereka.

  • Genesis 46:12
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 12 Ana a Yuda+ anali Ere,+ Onani,+ Shela,+ Perezi,+ ndi Zera.+ Komabe, Ere ndi Onani anafera kudziko la Kanani.+

      Ana a Perezi anali Hezironi+ ndi Hamuli.+

  • Genesis 49:10
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 10 Ndodo yachifumu sidzachoka kwa Yuda,+ ndiponso chibonga cha wolamulira sichidzachoka pakati pa mapazi ake, kufikira Silo*+ atabwera. Ndipo mitundu ya anthu idzamumvera.+

  • Numeri 2:3
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 3 “Chigawo cha mafuko atatu cha Yuda ndi asilikali awo, chizimanga msasa wawo kum’mawa kotulukira dzuwa. Mtsogoleri wa ana a Yuda ndi Naasoni,+ mwana wa Aminadabu.

  • 1 Mbiri 5:2
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 2 Chifukwa chakuti Yuda+ anali wamphamvu pakati pa abale ake, mwa iye munachokera mtsogoleri,+ koma udindo wa woyamba kubadwa unali wa Yosefe.+

  • Mateyu 1:2
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    •  2 Abulahamu anabereka Isaki.+

      Isaki anabereka Yakobo.+

      Yakobo anabereka Yuda+ ndi abale ake.

  • Aheberi 7:14
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 14 Tonse tikudziwa kuti Ambuye wathu anatuluka m’fuko la Yuda,+ ndipo ponena za fuko limeneli Mose sanatchulepo chilichonse chokhudza ansembe.

  • Chivumbulutso 5:5
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 5 Koma mmodzi wa akulu aja anandiuza kuti: “Tonthola. Taona! Mkango wa fuko la Yuda,+ muzu+ wa Davide,+ anapambana pa nkhondo+ moti iye ndiye woyenera kumatula zidindo 7 zimene amatira mpukutuwo ndi kuutsegula.”

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena