6 kapena zimene anachitira Datani ndi Abiramu,+ ana a Eliyabu, mwana wa Rubeni, pamene dziko linatsegula pakamwa pake ndi kuwameza pamodzi ndi mabanja awo, mahema awo, ndi chamoyo china chilichonse chimene chinali pakati pawo. Dziko linawameza ali pakati pa Aisiraeli onse).+