Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • Deuteronomo 4:34
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 34 Kapena kodi Mulungu anayamba wapitapo kukadzitengera mtundu wa anthu pakati pa mtundu wina ndi mayesero,+ zizindikiro,+ zozizwitsa,+ nkhondo,+ dzanja lamphamvu,+ mkono wotambasula,+ ndi zoopsa zazikulu+ zofanana ndi zimene Yehova Mulungu wanu anakuchitirani ku Iguputo inu mukuona?

  • Deuteronomo 7:19
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 19 Uzikumbukira mayesero aakulu amene maso ako anaona,+ zizindikiro, zozizwitsa+ ndiponso dzanja lamphamvu+ ndi mkono wotambasula+ umene Yehova Mulungu wako anakutulutsa nawo m’dzikolo.+ Umu ndi mmene Yehova Mulungu wako adzachitira ndi anthu a mitundu yonse amene ukuwaopa.+

  • Nehemiya 9:17
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 17 Choncho iwo anakana kumvera+ ndipo sanakumbukire+ zochita zanu zodabwitsa zimene munawachitira, m’malomwake anaumitsa khosi lawo+ ndipo anasankha mtsogoleri+ kuti awatsogolere pobwerera ku ukapolo wawo ku Iguputo. Koma inu ndinu Mulungu wokhululuka,+ wachisomo+ ndi wachifundo,+ wosakwiya msanga+ ndiponso wosonyeza kukoma mtima kosatha,+ chotero simunawasiye.+

  • Nehemiya 9:19
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 19 inuyo simunawasiye m’chipululu chifukwa cha chifundo chanu chachikulu.+ Mtambo woima njo ngati chipilala sunawachokere usana ndipo unali kuwatsogolera,+ ngakhalenso moto woima njo ngati chipilala sunawachokere usiku ndipo unali kuwaunikira njira imene anayenera kuyendamo.+

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena