Genesis 38:8 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 8 Yuda ataona zimenezi anauza Onani kuti: “Gona ndi mkazi wa m’bale wako ndipo uchite chokolo, kuti um’berekere ana m’bale wako.”+ Deuteronomo 25:6 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 6 Mwana woyamba amene mkaziyo angabereke, atenge dzina la mwamuna womwalira uja,+ kuti dzina la m’bale wake lisafafanizike mu Isiraeli.+ Rute 2:20 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 20 Pamenepo Naomi anauza mpongozi wakeyo kuti: “Yehova amene sanaleke kusonyeza kukoma mtima kosatha+ kwa amoyo ndi akufa,+ am’dalitse munthu ameneyu.”+ Ndipo Naomi anapitiriza kuti: “Munthuyutu ndi wachibale wathu.+ Ndi mmodzi wa otiwombola.”+ Rute 4:5 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 5 Kenako Boazi anati: “Ukadzagula mundawo kwa Naomi, ndiye kuti waugulanso kwa Rute Mmowabu, amene mwamuna wake anamwalira, kuti dzina la mwamuna wakeyo libwerere pacholowa chake.”+
8 Yuda ataona zimenezi anauza Onani kuti: “Gona ndi mkazi wa m’bale wako ndipo uchite chokolo, kuti um’berekere ana m’bale wako.”+
6 Mwana woyamba amene mkaziyo angabereke, atenge dzina la mwamuna womwalira uja,+ kuti dzina la m’bale wake lisafafanizike mu Isiraeli.+
20 Pamenepo Naomi anauza mpongozi wakeyo kuti: “Yehova amene sanaleke kusonyeza kukoma mtima kosatha+ kwa amoyo ndi akufa,+ am’dalitse munthu ameneyu.”+ Ndipo Naomi anapitiriza kuti: “Munthuyutu ndi wachibale wathu.+ Ndi mmodzi wa otiwombola.”+
5 Kenako Boazi anati: “Ukadzagula mundawo kwa Naomi, ndiye kuti waugulanso kwa Rute Mmowabu, amene mwamuna wake anamwalira, kuti dzina la mwamuna wakeyo libwerere pacholowa chake.”+