30Ndiyeno zimene zinachitika n’zakuti, pamene Davide ndi asilikali ake anali kubwerera ku Zikilaga+ tsiku lachitatu, Aamaleki+ anaukira anthu a kum’mwera* ndi a mumzinda wa Zikilaga ndi kufunkha zinthu zawo. Iwo anathira nkhondo mzindawo ndi kuutentha ndi moto.
12Tsopano nawa anthu amene anapita kwa Davide ku Zikilaga,+ pa nthawi imene iye sanali kuyenda momasuka chifukwa choopa Sauli+ mwana wa Kisi. Iwowa anali ena mwa amuna amphamvu+ amene anamuthandiza pankhondo.
20 Davide atapita ku Zikilaga,+ anthu ena a fuko la Manase anapita kumbali yake. Anthuwo anali Adinala, Yozabadi, Yediyaeli, Mikayeli, Yozabadi, Elihu, ndi Ziletai. Aliyense wa amenewa anali mtsogoleri+ wa asilikali 1,000, a fuko la Manase.