Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • 1 Samueli 14:6
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 6 Choncho Yonatani anauza mtumiki wake womunyamulira zida uja kuti: “Tiye tiwolokere kumudzi wa amuna osadulidwawa.+ Pakuti mwina Yehova adzatithandiza, chifukwa palibe chimene chingalepheretse Yehova kupulumutsa anthu ake pogwiritsa ntchito anthu ambiri kapena ochepa.”+

  • 1 Samueli 17:26
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 26 Ndiyeno Davide anayamba kufunsa amuna amene anali ataimirira pafupi naye kuti: “Kodi munthu amene angakaphe Mfilisiti+ ameneyu ndi kuchotsa chitonzo pa Isiraeli+ amuchitira chiyani? Kodi Mfilisiti wosadulidwa+ ameneyu ndani kuti azinyoza+ asilikali a Mulungu wamoyo?”+

  • 2 Samueli 1:20
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 20 Anthu inu musanene zimenezi mumzinda wa Gati.+

      Musalengeze zimenezi m’misewu ya Asikeloni,+

      Kuopera kuti ana aakazi a Afilisiti angasangalale,+

      Kuopera kuti ana aakazi a anthu osadulidwa angakondwere.

  • Ezekieli 44:7
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 7 Mumatenga alendo osachita mdulidwe wa mtima ndi mdulidwe wa khungu lawo+ kuti alowe m’malo anga opatulika ndi kuwadetsa. Ndithu iwo amadetsa nyumba yanga. Pamene mukupereka chakudya+ changa chomwe ndi mafuta+ ndi magazi,+ pangano langa limaphwanyidwa chifukwa cha zonyansa zanu zonse.+

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena