6 Atatero, Davide ndi Aisiraeli onse ananyamuka kupita ku Baala,+ ku Kiriyati-yearimu, amene ali m’dera la Yuda. Anapita kumeneko kukatenga likasa la Mulungu woona, Yehova, wokhala pa akerubi.+ Palikasa limeneli, amaitanirapo dzina lake.
4 Koma Davide anali atachotsa likasa+ la Mulungu woona ku Kiriyati-yearimu+ n’kukaliika kumalo amene iye anakonza,+ pakuti anali atamanga hema wa likasalo ku Yerusalemu.+