Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • Ekisodo 25:22
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 22 Ine ndidzaonekera kwa iwe pamenepo ndi kulankhula nawe kuchokera pamwamba pa chivundikiro,+ pakati pa akerubi awiriwo amene ali pamwamba pa likasa la umboni. Kuchokera pamenepo ndidzakulamula zonse zokhudza ana a Isiraeli.+

  • Numeri 7:89
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 89 Nthawi zonse Mose akalowa m’chihema chokumanako kukalankhula ndi Mulungu,+ anali kumva mawu kuchokera pamwamba pa likasa la umboni akulankhula naye. Mawuwo anali kuchokera pachivundikiro+ chimene chinali palikasa la umboni, pakati pa akerubi awiri.+ Mulungu anali kulankhula naye motero.

  • 1 Samueli 4:4
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 4 Motero anthuwo anatumiza anthu ku Silo kukatenga likasa la pangano la Yehova wa makamu, amene akukhala pa akerubi.+ Ndipo Hofeni ndi Pinihasi, ana awiri a Eli, anali pamenepo ndi likasa la pangano la Mulungu woona.+

  • 2 Samueli 6:2
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 2 Ndiyeno Davide ndi anthu onse amene anali naye ananyamuka ndi kupita ku Baale-yuda+ kuti akatenge likasa+ la Mulungu woona. Pa likasa limeneli amaitanira dzina+ la Yehova wa makamu,+ wokhala pamwamba pa akerubi.+

  • 2 Mafumu 19:15
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 15 Ndiyeno Hezekiya anayamba kupemphera+ pamaso pa Yehova, kuti: “Inu Yehova Mulungu wa Isiraeli+ wokhala pa akerubi,+ inu nokha ndinu Mulungu woona wa maufumu onse+ a padziko lapansi.+ Inuyo munapanga kumwamba+ ndi dziko lapansi.+

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena