24 Atangowatulutsa mafumuwo anapita nawo kwa Yoswa. Iye anaitana amuna onse a Isiraeli amene anapita naye kunkhondoko, n’kuuza atsogoleri awo kuti: “Bwerani kuno muponde kumbuyo kwa makosi a mafumuwa.”+ Iwo anabwera n’kupondadi kumbuyo kwa makosi awo.+