3 Anthu amene anali mumzindawo Davide anawatulutsa, ndipo anayamba kuwagwiritsa ntchito+ yocheka miyala, kusula zitsulo zakuthwa, ndiponso kusula nkhwangwa.+ Zimenezi n’zimene Davide anachitira mizinda yonse ya ana a Amoni. Pamapeto pake, Davide pamodzi ndi anthu onse anabwerera ku Yerusalemu.