Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • Genesis 27:1
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 27 Tsopano Isaki anakalamba moti maso ake sanali kuonanso.+ Ndiyeno anaitanitsa mwana wake wamkulu Esau,+ n’kumuuza kuti: “Mwana wanga!” Iye anayankha kuti: “Ine bambo!”

  • Genesis 48:10
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 10 Maso a Isiraeli anali atafooka chifukwa chokalamba,+ moti sankatha kuona. Yosefe anabweretsa anawo pafupi ndi bambo ake, ndipo bambo akewo anawapsompsona anawo n’kuwakumbatira.+

  • Deuteronomo 27:18
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 18 “‘Wotembereredwa ndi munthu wosocheretsa wakhungu.’+ (Anthu onse ayankhe kuti, ‘Zikhale momwemo!’)

  • 1 Samueli 3:2
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 2 Ndiyeno tsiku lina Eli anali atagona m’chipinda chake. Pa nthawiyi, maso ake anali atayamba kuchita mdima+ moti sanali kuona.

  • Salimo 90:10
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 10 Masiku a moyo wathu amangokwana zaka 70,+

      Ndipo ngati tili ndi mphamvu yapadera amakwana zaka 80.+

      Koma ngakhale zili choncho, amangodzaza ndi mavuto ndi zopweteka.+

      Pakuti masiku amene timakhala ndi moyo amatha mwamsanga ndipo timachoka mofulumira.+

  • Mlaliki 12:3
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 3 Pa nthawi imeneyo oyang’anira nyumba+ azidzanjenjemera, amuna amphamvu adzapindika,+ akazi opera ufa+ adzasiya kugwira ntchito chifukwa adzatsala ochepa, akazi oyang’ana pawindo+ azidzaona mdima,

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena