-
2 Mafumu 18:4Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
4 Hezekiya ndiye anachotsa malo okwezeka,+ kugwetsa zipilala zopatulika,+ ndi kudula mzati wopatulika.+ Iye anaphwanyaphwanya njoka yamkuwa+ imene Mose anapanga,+ chifukwa pofika masiku amenewo, ana a Isiraeli anakhala akufukiza nsembe+ yautsi kwa njoka yamkuwayo, ndipo inkatchedwa fano la njoka yamkuwa.+
-
-
2 Mbiri 34:4Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
4 Kuwonjezera apo, anthu anagwetsa maguwa ansembe+ a Abaala+ pamaso pake, ndipo zofukizira+ zimene zinali pamwamba pa maguwawo iye anazigumula. Mizati yopatulika,+ zifaniziro zogoba,+ ndi zifaniziro zopangidwa ndi zitsulo zosungunula, anaziphwanya n’kuziperapera.+ Phulusa lakelo analiwaza pamanda a anthu amene anali kupereka nsembe kwa zinthu zimenezi.+
-