2 Chotero patapita zaka, iye anapita kwa Ahabu ku Samariya.+ Ahabu anapha nkhosa ndi ng’ombe zambiri n’kuzipereka nsembe+ m’malo mwa Yehosafati ndi anthu amene anali naye. Kenako Ahabu anayamba kunyengerera+ Yehosafati kuti apite kukamenyana ndi mzinda wa Ramoti-giliyadi.+