30 “‘Ichi chidzakhala chizindikiro chanu: Chaka chino mudya mbewu zomera zokha zimene zinagwera pansi.+ Chaka chamawa mudzadya mbewu zongomera zokha, koma chaka chamkuja, anthu inu mudzabzale mbewu n’kukolola, ndipo mudzalime minda ya mpesa n’kudya zipatso zake.+