27 Ana a Isiraeli anasonkhana pamodzi n’kutenga zonse zofunikira+ ndipo ananyamuka kupita kukakumana nawo. Ana a Isiraeliwo anamanga msasa kutsogolo kwa Asiriya. Iwo anali ngati timagulu tiwiri ting’onoting’ono ta mbuzi pamene Asiriyawo anadzaza dziko lonse.+