40 Onsewa anali ana a Aseri, atsogoleri+ a nyumba ya makolo awo, amuna ochita kusankhidwa, amphamvu ndi olimba mtima.+ Iwo anali akuluakulu a atsogoleri, ndipo mndandanda wa mayina awo+ anaugwiritsa ntchito powalemba usilikali, pokonzekera nkhondo. Analipo amuna 26,000.+