4 Mu Yerusalemu munalinso kukhala ena mwa ana a Yuda ndi ena mwa ana a Benjamini.+ Mwa ana a Yuda panali Ataya mwana wamwamuna wa Uziya amene anali mwana wa Zekariya. Zekariya anali mwana wa Amariya, Amariya anali mwana wa Sefatiya, Sefatiya anali mwana wa Mahalalele wochokera m’banja la Perezi.+