49 Aroni+ ndi ana ake anali kufukiza nsembe yautsi+ paguwa lansembe zopsereza+ ndi paguwa lansembe zofukiza+ kuti akwaniritse ntchito zonse zokhudzana ndi zinthu zopatulika kwambiri, ndiponso kuti aphimbe machimo+ a Aisiraeli,+ malinga ndi zonse zimene Mose mtumiki wa Mulungu woona analamula.