8 Kuchigawo chakum’mawa kwa Yorodano, m’dera la kufupi ndi Yeriko, kunali Bezeri+ m’chipululu cha m’dera lokwererapo la fuko la Rubeni.+ Kunalinso Ramoti+ ku Giliyadi m’dera la fuko la Gadi, ndi Golani+ ku Basana m’dera la fuko la Manase.
2 Chotero patapita zaka, iye anapita kwa Ahabu ku Samariya.+ Ahabu anapha nkhosa ndi ng’ombe zambiri n’kuzipereka nsembe+ m’malo mwa Yehosafati ndi anthu amene anali naye. Kenako Ahabu anayamba kunyengerera+ Yehosafati kuti apite kukamenyana ndi mzinda wa Ramoti-giliyadi.+