10Mfumukazi ya ku Sheba+ inali kumva za Solomo, ndi zoti anatchuka chifukwa cha dzina la Yehova.+ Choncho inabwera kuti idzamuyese pomufunsa mafunso ovuta.+
42 Mfumukazi ya kum’mwera+ adzaiukitsa kwa akufa limodzi ndi m’badwo uwu ndipo idzautsutsa, chifukwa mfumukazi imeneyi inabwera kuchokera kumalekezero a dziko lapansi kudzamva nzeru za Solomo. Koma tsopano wina woposa Solomo ali pano.+
31 Mfumukazi+ ya kum’mwera adzaiimiritsa pa chiweruzo limodzi ndi anthu a m’badwo uwu, ndipo idzawatsutsa. Chifukwa mfumukazi imeneyi inabwera kuchokera kumalekezero a dziko lapansi kudzamva nzeru za Solomo. Koma tsopano wina woposa+ Solomo ali pano.