9 Kuchokera kwa Rehumu+ mtsogoleri wa akulu a boma, Simusai mlembi, anzawo ena onse monga oweruza ndi abwanamkubwa aang’ono a kutsidya lina la Mtsinje,*+ alembi+ ena, anthu a ku Ereke,+ Ababulo,+ anthu okhala ku Susa,+ kapena kuti Aelamu,+
15 Amtokomawo anapita mofulumira+ chifukwa cha mawu a mfumu ndi lamulo limene linaperekedwa m’nyumba ya mfumu yokhala ndi mpanda wolimba kwambiri ya ku Susani.+ Ndipo mfumu ndi Hamani, anakhala pansi kuti amwe vinyo,+ koma mumzinda wa Susani+ munali chipwirikiti.+
2 Nditayamba kuona masomphenyawo ndinapezeka kuti ndili kunyumba ya mfumu yokhala ndi mpanda wolimba kwambiri ya ku Susani,+ imene ili m’chigawo cha Elamu.+ M’masomphenyawo ndinapezeka kuti ndili m’mphepete mwa mtsinje wa Ulai.+