19 Kodi zoona mukundinyozetsa pamaso pa anthu anga chifukwa cha balere wongodzaza m’manja ndi nyenyeswa za mkate?+ Kodi mukuphadi anthu osayenera kufa,+ ndipo mukusiya anthu osayenera kukhala ndi moyo, ponamiza anthu anga amene akumva bodza lanulo?”’+