10 Ansembe onyamula Likasawo, anaimabe chiimire pakati+ pa mtsinje wa Yorodano, kufikira zitachitika zonse zimene Yehova analamula Yoswa kuti auze anthuwo, mogwirizana ndi zonse zimene Mose analamula Yoswa.+ Ansembewo ali chiimire choncho, anthuwo anawoloka mtsinjewo mofulumira.+