30 “‘Chakhumi* chilichonse+ cha zinthu za m’dzikolo, kaya ndi zokolola m’munda kapena zipatso za m’mitengo, ndi cha Yehova. Chakhumi chimenechi ndi chopatulika kwa Yehova.
21 “Kunena za ana a Levi, iwo ndawapatsa chakhumi+ chilichonse mu Isiraeli monga cholowa chawo chifukwa cha utumiki wawo umene akuchita, utumiki wa pachihema chokumanako.