-
Nehemiya 10:37Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
37 Komanso tinafunika kupititsa ufa woyambirira wamisere,+ zopereka zathu,+ zipatso za mtengo uliwonse,+ vinyo watsopano+ ndi mafuta+ kwa ansembe kumalo odyera+ m’nyumba ya Mulungu wathu. Tinafunikanso kupititsa chakhumi kwa Alevi+ pa zinthu zochokera m’nthaka yathu, pakuti Aleviwo anali kulandira chakhumi kuchokera m’mizinda yathu yonse ya zaulimi.
-
-
Nehemiya 12:44Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
44 Kuwonjezera apo, pa tsiku limenelo anaika amuna kuti aziyang’anira zipinda+ zosungiramo zinthu zosiyanasiyana,+ zopereka,+ mbewu zoyambirira+ ndi chakhumi.+ Anawapatsa udindo wosonkhanitsira m’zipindamo gawo loyenera kuperekedwa kwa ansembe ndi Alevi+ malinga ndi chilamulo,+ kuchokera m’minda yonse ya m’mizinda yawo. Yuda anali kusangalala chifukwa ansembe ndi Alevi+ anali kuchita utumiki wawo.
-