2 Ndiyeno Haneni+ mmodzi mwa abale anga anabwera pamodzi ndi amuna ena kuchokera ku Yuda. Ndinawafunsa+ mmene zinthu zinalili kwa gulu la Ayuda+ amene anathawa+ ku ukapolo+ komanso ndinawafunsa za Yerusalemu.
5 Tsopano mwamuna wina, Myuda, anali kunyumba ya mfumu yokhala ndi mpanda wolimba kwambiri ya ku Susani.+ Mwamunayu dzina lake anali Moredekai+ mwana wa Yairi, mwana wa Simeyi amene anali mwana wa Kisi M’benjamini.+