-
Esitere 9:27Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
27 Ayudawo anaika lamulo ndi kuvomereza kuti iwo, ana awo ndi anthu onse odziphatika kwa iwo+ adzatsatira lamuloli. Lamuloli linali lakuti, nthawi zonse azisunga masiku awiri amenewa mogwirizana ndi zimene zinalembedwa zokhudza masikuwa komanso kuti aziwasunga pa nthawi yoikidwiratu chaka ndi chaka.
-