Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • Yobu 5:10
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 10 Kwa Iye amene amapereka mvula padziko lapansi,+

      Ndi kupititsa madzi pabwalo.+

  • Yobu 26:8
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    •  8 Iye anakulunga madzi m’mitambo yake,+

      Moti mitamboyo sing’ambika pansi pa madziwo.

  • Yobu 37:10
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 10 Mpweya wa Mulungu umapereka madzi oundana,+

      Ndipo malo aakulu a madzi ndi oundana.+

  • Miyambo 30:4
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 4 Ndani amene anakwerapo kumwamba n’kubwerako?+ Ndani anasonkhanitsapo mphepo m’manja mwake?+ Ndani anamangapo madzi munsalu?+ Ndani anaika malekezero onse a dziko lapansi?+ Dzina lake ndani?+ Nanga mwana wake dzina lake ndani? Ndiuzeni ngati mukudziwa.+

  • Yesaya 40:12
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 12 Ndani anayezapo madzi onse a m’nyanja pachikhatho cha dzanja lake?+ Ndani anayezapo kumwamba konse ndi dzanja lake?+ Ndani anayezapo fumbi lonse la padziko lapansi ndi mbale imodzi yokha yoyezera?+ Ndani anayezapo mapiri ndi muyezo, kapena ndani anayezapo zitunda pa sikelo?

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena