Miyambo 15:23 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 23 Munthu amasangalala ndi yankho lochokera pakamwa pake,+ ndipo mawu onenedwa pa nthawi yoyenera ndi abwino kwambiri.+ Miyambo 24:26 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 26 Woyankha mosapita m’mbali adzapsompsona milomo ya anthu.+ Mlaliki 12:10 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 10 Wosonkhanitsayo anafufuza mawu okoma+ ndipo analemba mawu olondola a choonadi.+ Yesaya 50:4 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 4 Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, wandipatsa lilime la anthu ophunzitsidwa bwino+ kuti ndidziwe mmene ndingamuyankhire munthu wotopa.+ Iye amandidzutsa m’mawa uliwonse. Amandidzutsa kuti makutu anga amve ngati anthu ophunzitsidwa bwino.+
23 Munthu amasangalala ndi yankho lochokera pakamwa pake,+ ndipo mawu onenedwa pa nthawi yoyenera ndi abwino kwambiri.+
4 Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, wandipatsa lilime la anthu ophunzitsidwa bwino+ kuti ndidziwe mmene ndingamuyankhire munthu wotopa.+ Iye amandidzutsa m’mawa uliwonse. Amandidzutsa kuti makutu anga amve ngati anthu ophunzitsidwa bwino.+