Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • Deuteronomo 24:5
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 5 “Mwamuna akatenga mkazi watsopano,+ sayenera kukhala m’gulu lankhondo, ndiponso asakakamizidwe kuchita china chilichonse. Akhale kunyumba osachita zinthu zimenezi kwa chaka chimodzi kuti asangalatse mkazi amene watenga.+

  • Mlaliki 9:9
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 9 Sangalala ndi moyo limodzi ndi mkazi wako amene umamukonda+ masiku onse a moyo wako wachabechabe, amene Mulungu wakupatsa padziko lapansi pano. Usangalale masiku ako onse achabechabe, pakuti imeneyo ndiyo mphoto yako pamoyo,+ ndi pa ntchito yovuta imene ukuigwira mwakhama padziko lapansi pano.

  • Malaki 2:15
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 15 Komabe pakati panu pali ena amene atsimikiza mtima kuti asachite zoterezi. Iwo akufuna kukhala ndi ana amene angakhaledi anthu a Mulungu.*+ Mphamvu ya Mulungu ikutsogolera anthu amenewa pa zonse zimene akuchita. Tsopano inunso ganizirani mofatsa ndipo mukhale ndi maganizo oyenera.+ Tsimikizani mtima kuti musachitire zachinyengo akazi anu amene munawakwatira muli anyamata.+

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena