10 Usachite mantha ndi mavuto amene ukumane nawo.+ Taona! Mdyerekezi+ adzapitiriza kuponya m’ndende ena a inu, kuti muyesedwe mpaka pamapeto,+ ndipo mudzakhala m’masautso+ masiku 10. Sonyeza kukhulupirika kwako mpaka imfa,+ ndipo ndidzakupatsa mphoto ya moyo.+