8 Tsopano pakati pa anthuwo panali amuna 10 amene anauza Isimaeli mofulumira kuti: “Usatiphe, pakuti tili ndi chuma chobisika m’munda. Tili ndi tirigu, barele, mafuta ndi uchi.”+ Chotero Isimaeli anawasiya ndipo sanawaphe mmene anachitira ndi abale awo.