Yobu 40:12 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 12 Uone wodzikweza aliyense n’kumuchepetsa,+Ndipo oipa uwaponderezere pamalo pomwe alilipo. Miyambo 6:17 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 17 Maso odzikweza,+ lilime lonama,+ manja okhetsa magazi a anthu osalakwa,+ Miyambo 8:13 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 13 Kuopa Yehova kumatanthauza kudana ndi zoipa.+ Ndimadana ndi kudzikweza, kunyada,+ njira yoipa ndiponso pakamwa ponena zopotoka.+ Miyambo 21:4 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 4 Maso odzikweza ndi mtima wodzikuza+ ndizo nyale ya anthu oipa, ndipo zimenezi ndi tchimo.+
13 Kuopa Yehova kumatanthauza kudana ndi zoipa.+ Ndimadana ndi kudzikweza, kunyada,+ njira yoipa ndiponso pakamwa ponena zopotoka.+