Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • Yesaya 57:19
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 19 “Ndikulenga chipatso cha milomo.+ Mtendere wosatha udzakhala kwa yemwe ali kutali ndiponso kwa yemwe ali pafupi,+ ndipo ndidzam’chiritsa,”+ akutero Yehova.

  • Ezekieli 34:25
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 25 “‘“Ine ndidzachita nazo pangano la mtendere.+ Ndidzachotsa zilombo zolusa zakutchire m’dzikomo.+ Nkhosazo zidzakhala m’chipululu popanda choziopsa ndipo zizidzagona m’nkhalango.+

  • Hoseya 2:18
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 18 Pa tsiku limenelo ndidzachita pangano ndi chilombo chakuthengo,+ cholengedwa chouluka m’mlengalenga ndi cholengedwa chokwawa panthaka, kuti ndithandize anthu anga. Ndidzathyola uta ndi lupanga ndipo ndidzathetsa nkhondo padziko.+ Pamenepo ndidzawachititsa kukhala mwabata.+

  • Aroma 5:1
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 5 Chotero, popeza tsopano tayesedwa olungama chifukwa chokhala ndi chikhulupiriro,+ tiyeni tikhale pa mtendere+ ndi Mulungu kudzera mwa Ambuye wathu Yesu Khristu.

  • 2 Akorinto 5:19
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 19 Utumiki wake ndi woti tilengeze kuti Mulungu anali kugwirizanitsa dziko+ ndi iyeyo+ kudzera mwa Khristu,+ moti sanawawerengere anthuwo machimo awo,+ ndipo watipatsa ifeyo ntchito yolengeza uthenga+ umenewu wokhazikitsanso mtendere.+

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena