13 Inu mumanena kuti, ‘Koma ndiye n’zotopetsa bwanji!’+ Ndipo mumanunkhiza nsembezo monyansidwa,” watero Yehova wa makamu. “Inu mumabweretsa nyama zobedwa, zolumala ndi zodwala.+ Mumapereka zimenezi ngati mphatso. Kodi zopereka zanu zoterezi ine ndingakondwere nazo?”+ watero Yehova.