Malaki
3 “Taonani! Ine nditumiza mthenga wanga+ ndipo iye adzandikonzera njira.+ Mwadzidzidzi, Ambuye woona, amene anthu inu mukumufunafuna, adzabwera kukachisi+ Wake.+ Adzabwera ndi mthenga+ wa pangano+ amene mukumuyembekezera mosangalala.+ Iye adzabwera ndithu,” watero Yehova wa makamu.+
2 “Ndani adzapirire pa tsiku limene adzabwere?+ Ndipo ndani adzaime chilili iye akadzaonekera?+ Iye adzakhala ngati moto wa woyenga zitsulo+ komanso ngati sopo+ wa ochapa zovala.+ 3 Iye adzakhala pansi ngati woyenga zitsulo ndiponso ngati woyeretsa siliva.+ Adzayeretsa ana a Levi+ ndipo adzawayeretsa ngati golide+ ndi siliva. Pamene azidzapereka nsembe zawo ngati mphatso, Yehova adzaona kuti nsembe zawozo akuzipereka+ molungama. 4 Nsembe zimene Yuda ndi Yerusalemu adzapereke monga mphatso, zidzasangalatsa Yehova,+ ngati mmene zinalili kalekale kapena kuti nthawi zamakedzana.+
5 “Anthu inu ndidzakuyandikirani kuti ndikuweruzeni.+ Sindidzazengereza kupereka umboni+ wotsutsa amatsenga,+ achigololo,+ olumbira monama+ komanso ochita chinyengo pa malipiro a munthu waganyu.+ Sindidzazengereza kupereka umboni wotsutsa anthu ochitira chinyengo mkazi wamasiye,+ mwana wamasiye*+ ndiponso opondereza alendo.+ Anthu amenewa sakundiopa,”+ watero Yehova wa makamu.
6 “Ine ndine Yehova, sindinasinthe.+ Inu ndinu ana a Yakobo ndipo simunatheretu.+ 7 Kuyambira m’masiku a makolo anu mwakhala mukupatuka pa malamulo anga ndipo simunawasunge.+ Bwererani kwa ine ndipo ine ndibwerera kwa inu,”+ watero Yehova wa makamu.
Koma inu mukunena kuti: “Tibwerere motani?”
8 “Kodi munthu wochokera kufumbi angabere Mulungu? Komatu inu mukundibera.”
Inu mukunena kuti: “Takuberani motani?”
“Mukundibera kudzera m’chakhumi* ndi m’zopereka. 9 Inu mukundinyoza kwambiri+ ndipo mukundibera. Mtundu wanu wonsewu ukuchita zimenezi. 10 Bweretsani gawo limodzi mwa magawo 10 alionse a zinthu zanu+ n’kuziika mosungiramo zinthu zanga, kuti m’nyumba mwanga mukhale chakudya.+ Ndiyeseni chonde pa nkhani imeneyi,+ kuti muone ngati sindidzakutsegulirani zipata za kumwamba+ ndi kukukhuthulirani madalitso oti mudzasowa powalandirira,”+ watero Yehova wa makamu.
11 “Ine ndidzakudzudzulirani dzombe,+ ndipo silidzawononganso mbewu za m’munda mwanu. Mitengo ya mpesa ya m’munda mwanu izidzabereka zipatso nthawi zonse,”+ watero Yehova wa makamu.
12 “Mitundu ina yonse ya anthu idzakutchani odala,+ pakuti mudzakhala dziko losangalatsa,”+ watero Yehova wa makamu.
13 “Inu mwandinenera mawu achipongwe,”+ watero Yehova.
Koma mukunena kuti: “Ife takunenerani zachipongwe zotani?”+
14 “Inu mwanena kuti, ‘Kutumikira Mulungu n’kopanda phindu.+ Tapindulanji chifukwa chomutumikira ndiponso chifukwa choyenda mwachisoni pamaso pa Yehova wa makamu?+ 15 Panopa anthu odzikuza tikuwatcha odala.+ Komanso anthu ochita zoipa zinthu zikuwayendera bwino.+ Iwo ayesa Mulungu koma sakulandira chilango.’”+
16 Pa nthawi imeneyo anthu oopa Yehova+ analankhulana, aliyense ndi mnzake, ndipo Yehova anatchera khutu ndi kumvetsera.+ Buku la chikumbutso linayamba kulembedwa pamaso pake.+ Buku limeneli linali lonena za anthu oopa Yehova ndi anthu amene anali kuganizira za dzina lake.+
17 “Iwo adzakhala anthu anga,+ pa tsiku limene ndidzawasandutse chuma chapadera,”+ watero Yehova wa makamu. “Ndidzawachitira chifundo monga mmene munthu amachitira chifundo mwana wake amene amamutumikira.+ 18 Ndithu, anthu inu mudzaonanso kusiyana pakati pa munthu wolungama ndi woipa+ ndiponso pakati pa munthu amene akutumikira Mulungu ndi amene sanatumikirepo Mulungu.”+