Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • Genesis 1:27
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 27 Motero Mulungu analenga munthu m’chifaniziro chake,+ m’chifaniziro cha Mulungu anam’lenga iye. Anawalenga mwamuna ndi mkazi.+

  • Genesis 2:7
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 7 Kenako, Yehova Mulungu anaumba munthu kuchokera kufumbi lapansi,+ ndipo anauzira mpweya wa moyo+ m’mphuno mwake, munthuyo n’kukhala wamoyo.+

  • Genesis 5:2
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 2 Anawalenga iwo mwamuna ndi mkazi.+ Kenako, anawadalitsa ndi kuwatchula dzina lakuti Anthu,+ m’tsiku limene anawalenga.+

  • Deuteronomo 4:32
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 32 “Tafunsani tsopano, za masiku akale+ inu musanakhalepo, kuchokera pa tsiku limene Mulungu analenga munthu padziko lapansi,+ ndiponso kuchokera kumalekezero ena a thambo kukafika kumalekezero ena a thambo, Kodi chinthu chachikulu ngati chimenechi chinayamba chachitikapo, kapena kodi chinthu ngati chimenechi chinayamba chamvekapo?+

  • Salimo 139:14
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 14 Ndidzakutamandani chifukwa munandipanga modabwitsa ndipo zimenezi zimandichititsa mantha.+

      Ntchito zanu ndi zodabwitsa,+

      Ndipo ine ndimadziwa bwino zimenezi.+

  • Yeremiya 27:5
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 5 ‘Ine ndinapanga dziko lapansi,+ anthu+ ndi nyama+ zapadziko lapansi pogwiritsa ntchito mphamvu zanga zazikulu+ ndiponso dzanja langa lotambasula.+ Ndipo dzikoli ndalipereka kwa amene ndikufuna.+

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena