Yesaya 48:17 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 17 Yehova, Wokuwombolani,+ Woyera wa Isiraeli,+ wanena kuti: “Ine Yehova ndine Mulungu wanu, amene ndimakuphunzitsani kuti zinthu zikuyendereni bwino,+ amene ndimakuchititsani kuti muyende m’njira imene muyenera kuyendamo.+ Yesaya 49:26 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 26 Amene akukuzunza ndidzawachititsa kuti adye mnofu wawo womwe, ndipo adzaledzera ndi magazi awo omwe ngati kuti amwa vinyo wotsekemera. Anthu onse ndithu adzadziwa kuti ine, Yehova,+ ndine Mpulumutsi wako+ ndiponso Wokuwombola,+ Wamphamvu wa Yakobo.”+
17 Yehova, Wokuwombolani,+ Woyera wa Isiraeli,+ wanena kuti: “Ine Yehova ndine Mulungu wanu, amene ndimakuphunzitsani kuti zinthu zikuyendereni bwino,+ amene ndimakuchititsani kuti muyende m’njira imene muyenera kuyendamo.+
26 Amene akukuzunza ndidzawachititsa kuti adye mnofu wawo womwe, ndipo adzaledzera ndi magazi awo omwe ngati kuti amwa vinyo wotsekemera. Anthu onse ndithu adzadziwa kuti ine, Yehova,+ ndine Mpulumutsi wako+ ndiponso Wokuwombola,+ Wamphamvu wa Yakobo.”+