1 Samueli 15:22 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 22 Poyankha Samueli anati: “Kodi Yehova amakondwera ndi nsembe zopsereza+ ndi nsembe zina kuposa kumvera mawu a Yehova? Taona! Kumvera+ kuposa nsembe,+ ndipo kumvetsera mosamala kuposa mafuta+ a nkhosa zamphongo. Salimo 40:6 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 6 Nsembe ndiponso zopereka, simunasangalale nazo.+Inu munatsegula makutu anga.+Simunapemphe nsembe yopsereza ndi nsembe yamachimo.+ Salimo 51:16 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 16 Pakuti nsembe singakusangalatseni, chifukwa ikanakusangalatsani ndikanaipereka kwa inu.+Nsembe yopsereza yathunthu singakusangalatseni.+ Miyambo 15:8 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 8 Nsembe ya anthu oipa imam’nyansa Yehova,+ koma pemphero la anthu owongoka mtima limam’sangalatsa.+ Mateyu 9:13 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 13 Choncho pitani mukaphunzire tanthauzo la mawu akuti, ‘Ndikufuna chifundo, osati nsembe.’+ Chifukwa ine sindinabwere kudzaitana anthu olungama, koma ochimwa.”
22 Poyankha Samueli anati: “Kodi Yehova amakondwera ndi nsembe zopsereza+ ndi nsembe zina kuposa kumvera mawu a Yehova? Taona! Kumvera+ kuposa nsembe,+ ndipo kumvetsera mosamala kuposa mafuta+ a nkhosa zamphongo.
6 Nsembe ndiponso zopereka, simunasangalale nazo.+Inu munatsegula makutu anga.+Simunapemphe nsembe yopsereza ndi nsembe yamachimo.+
16 Pakuti nsembe singakusangalatseni, chifukwa ikanakusangalatsani ndikanaipereka kwa inu.+Nsembe yopsereza yathunthu singakusangalatseni.+
13 Choncho pitani mukaphunzire tanthauzo la mawu akuti, ‘Ndikufuna chifundo, osati nsembe.’+ Chifukwa ine sindinabwere kudzaitana anthu olungama, koma ochimwa.”