2 Ayi si choncho. Koma zolakwa za anthu inu n’zimene zakulekanitsani ndi Mulungu wanu,+ ndipo machimo anu amuchititsa kuti akubisireni nkhope yake, kuti asamve zimene mukunena.+
4 Pa nthawiyo adzafuulira Yehova kuti awathandize, koma sadzawayankha.+ Adzawabisira nkhope yake pa nthawi imeneyo+ chifukwa cha zoipa zimene anali kuchita.+