Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • Deuteronomo 31:17
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 17 Pamenepo mkwiyo wanga udzawayakira tsiku limenelo,+ ndipo ndidzawasiya+ ndi kuwabisira nkhope yanga,+ motero adzakhala chinthu choyenera kuwonongedwa. Masoka ndi zowawa zambiri zidzawagwera,+ ndipo pa tsiku limenelo adzanena kuti, ‘Masoka amenewatu akutigwera chifukwa chakuti Mulungu wathu sali pakati pathu.’+

  • Deuteronomo 32:20
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 20 Choncho iye anati, ‘Ndiwabisire nkhope yanga,+

      Ndione kuti ziwathera bwanji.

      Pakuti iwo ndi m’badwo wokonda zoipa,+

      Ana osakhulupirika.+

  • Yesaya 57:17
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 17 “Ine ndinakwiya chifukwa cha phindu lachinyengo limene analipeza mosayenera.+ Ndinakwiya ndipo ndinamulanga. Ndinabisa nkhope yanga chifukwa cha mkwiyo.+ Koma iye ankangoyendabe ngati wopanduka+ m’njira ya mtima wake.

  • Ezekieli 39:23
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 23 Anthu a mitundu ina adzadziwa kuti a nyumba ya Isiraeli anatengedwa kupita ku ukapolo chifukwa cha zolakwa zawo.+ Adzadziwa kuti anali kundichitira zinthu zosakhulupirika. N’chifukwa chake ine ndinawabisira nkhope yanga+ n’kuwapereka m’manja mwa adani awo ndipo onsewo anaphedwa ndi lupanga.+

  • Mika 3:4
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 4 Pa nthawiyo adzafuulira Yehova kuti awathandize, koma sadzawayankha.+ Adzawabisira nkhope yake pa nthawi imeneyo+ chifukwa cha zoipa zimene anali kuchita.+

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena