Yesaya 30:27 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 27 Taonani! Dzina la Yehova likubwera kuchokera kutali. Likubwera ndi mkwiyo woyaka+ ndiponso mitambo yolemera. Pamilomo yake padzaza mawu odzudzula ndipo lilime lake lili ngati moto wowononga.+ Yeremiya 5:14 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 14 Chotero Yehova, Mulungu wa makamu wanena kuti: “Pakuti iwo akunena zimenezi, ndichititsa mawu anga m’kamwa mwako kukhala ngati moto+ koma anthu awa adzakhala ngati nkhuni ndipo motowo udzawanyeketsa.”+ Yeremiya 20:9 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 9 Choncho ndinanena kuti: “Sindidzanenanso za iye ndipo sindidzalankhulanso m’dzina lake.”+ Koma mumtima mwangamu, mawu ake anali ngati moto woyaka. Anali ngati moto woyaka umene autsekera m’mafupa anga. Choncho ndinatopa ndi kudziletsa kuti ndisalankhule moti sindinathenso kupirira.+
27 Taonani! Dzina la Yehova likubwera kuchokera kutali. Likubwera ndi mkwiyo woyaka+ ndiponso mitambo yolemera. Pamilomo yake padzaza mawu odzudzula ndipo lilime lake lili ngati moto wowononga.+
14 Chotero Yehova, Mulungu wa makamu wanena kuti: “Pakuti iwo akunena zimenezi, ndichititsa mawu anga m’kamwa mwako kukhala ngati moto+ koma anthu awa adzakhala ngati nkhuni ndipo motowo udzawanyeketsa.”+
9 Choncho ndinanena kuti: “Sindidzanenanso za iye ndipo sindidzalankhulanso m’dzina lake.”+ Koma mumtima mwangamu, mawu ake anali ngati moto woyaka. Anali ngati moto woyaka umene autsekera m’mafupa anga. Choncho ndinatopa ndi kudziletsa kuti ndisalankhule moti sindinathenso kupirira.+