Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • Deuteronomo 32:22
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 22 Pakuti pa kukwiya kwanga moto wayaka,+

      Ndipo udzayaka mpaka kukafika ku Manda,* malo a pansi penipeni.+

      Udzanyeketsa dziko lapansi ndi zipatso zake,+

      Ndi kuyatsa maziko a mapiri.+

  • Salimo 79:5
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    •  5 Haa! Inu Yehova, mukhala wokwiya mpaka liti? Kwamuyaya?+

      Kodi mkwiyo wanu udzakhala ukuyaka ngati moto mpaka liti?+

  • Yesaya 10:17
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 17 Kuwala kwa Isiraeli+ kudzasanduka moto+ ndipo Woyera wake adzasanduka lawi la moto.+ Iye adzayaka n’kunyeketsa udzu wake* ndi zitsamba zake zaminga+ pa tsiku limodzi.

  • Nahumu 1:6
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 6 Iye atapsa mtima, ndani angaime pamaso pake?+ Iye atakwiya, ndani angalimbe mtima kuima pamaso pake?+

      Mkwiyo wake adzaukhuthula ngati moto+ ndipo miyala idzagwetsedwa chifukwa cha iye.

  • Zefaniya 3:8
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 8 “‘Choncho pitirizani kundiyembekezera,’+ watero Yehova, ‘mpaka tsiku limene ndidzanyamuka kuti ndikaukire ndi kulanda zinthu zofunkhidwa.+ Chigamulo changa ndicho kusonkhanitsa mitundu ya anthu+ ndi kusonkhanitsa pamodzi maufumu kuti ndiwadzudzule mwamphamvu+ ndi kuwatsanulira mkwiyo wanga wonse woyaka moto, pakuti moto wa mkwiyo wanga udzanyeketsa dziko lonse lapansi.+

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena