Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • Ekisodo 6:1
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 6 Ndiyeno Yehova anauza Mose kuti: “Tsopano uona zimene ndichite kwa Farao.+ Chifukwa cha dzanja lamphamvu, iye awalola kuchoka, ndipo chifukwa cha dzanja lamphamvu awatulutsa m’dziko lake.”+

  • Ekisodo 15:16
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 16 Adzaopa ndipo adzagwidwa ndi mantha aakulu.+

      Chifukwa cha dzanja lanu lamphamvu, adzakhala chete ngati mwala.

      Kufikira anthu anu+ atadutsa, inu Yehova,

      Kufikira anthu anu amene munawapanga+ atadutsa.+

  • Deuteronomo 26:8
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 8 Pamapeto pake Yehova anatitulutsa mu Iguputo ndi dzanja lamphamvu+ ndi mkono wotambasula,+ zoopsa zazikulu,+ zizindikiro ndi zozizwitsa.+

  • 1 Mbiri 17:21
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 21 Ndi mtundu winanso uti padziko lapansi umene ungafanane ndi mtundu wa anthu anu Aisiraeli,+ amene inu Mulungu woona munawawombola monga anthu anu,+ ndi kudzipangira dzina mwa kuchita zinthu zazikulu+ ndi zochititsa mantha, popitikitsa mitundu+ pamaso pa anthu anu amene munawawombola ku Iguputo?

  • Salimo 136:12
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 12 Anawatulutsa ndi dzanja lamphamvu ndi mkono wotambasula:+

      Pakuti kukoma mtima kwake kosatha kudzakhalapobe mpaka kalekale.

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena