Deuteronomo 5:29 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 29 Zikanakhala bwino kwambiri akanakhala ndi mtima wondiopa+ ndi kusunga malamulo anga+ nthawi zonse, kuti iwo ndi ana awo zinthu ziwayendere bwino mpaka kalekale!*+ Yeremiya 6:8 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 8 Iwe Yerusalemu, mvera chilango+ kuti ndisatembenuke ndi kukufulatira chifukwa chonyansidwa nawe,+ kuti ndisakusandutse bwinja, dziko lopanda munthu aliyense wokhalamo.”+ Yeremiya 7:3 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 3 Yehova wa makamu, Mulungu wa Isiraeli wanena kuti: “Konzani njira zanu ndiponso zochita zanu kuti zikhale zabwino, ndipo ndidzachititsa anthu inu kukhalabe m’dziko lino.+ Yeremiya 9:12 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 12 “Kodi wanzeru ndani kuti amvetse zimenezi, kapenanso ndani amene Yehova wamulankhula kuti anene zimenezi?+ N’chifukwa chiyani dzikoli lidzawonongedwa ndiponso kutenthedwa n’kukhala ngati chipululu chopanda munthu wodutsamo?”+ Yeremiya 32:33 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 33 Iwo anali kundifulatira, sanandiyang’ane.+ Ngakhale kuti ndinali kuwaphunzitsa, kudzuka m’mawa kwambiri ndi kuwaphunzitsa, palibe ngakhale mmodzi wa iwo amene anamvetsera kuti alandire mwambo.*+
29 Zikanakhala bwino kwambiri akanakhala ndi mtima wondiopa+ ndi kusunga malamulo anga+ nthawi zonse, kuti iwo ndi ana awo zinthu ziwayendere bwino mpaka kalekale!*+
8 Iwe Yerusalemu, mvera chilango+ kuti ndisatembenuke ndi kukufulatira chifukwa chonyansidwa nawe,+ kuti ndisakusandutse bwinja, dziko lopanda munthu aliyense wokhalamo.”+
3 Yehova wa makamu, Mulungu wa Isiraeli wanena kuti: “Konzani njira zanu ndiponso zochita zanu kuti zikhale zabwino, ndipo ndidzachititsa anthu inu kukhalabe m’dziko lino.+
12 “Kodi wanzeru ndani kuti amvetse zimenezi, kapenanso ndani amene Yehova wamulankhula kuti anene zimenezi?+ N’chifukwa chiyani dzikoli lidzawonongedwa ndiponso kutenthedwa n’kukhala ngati chipululu chopanda munthu wodutsamo?”+
33 Iwo anali kundifulatira, sanandiyang’ane.+ Ngakhale kuti ndinali kuwaphunzitsa, kudzuka m’mawa kwambiri ndi kuwaphunzitsa, palibe ngakhale mmodzi wa iwo amene anamvetsera kuti alandire mwambo.*+